Mawu otsogolera

Kuyambira mchaka cha 2009, pachitika zinthu zambiri zopititsa patsogolo ntchito yokwaniritsa pangano la Mayiko Onse Padziko la Pansi Lokhudza Ufulu Wosiyanasiyana wa Anthu Olumala (United Nations Convention on the Rights of Persons with Disabilities (UNCRPD), Ntchitoyi ikupitilira kukonza ndi kulimbikitsa malamulo, ndondomeko, ndi ntchito zolimbikitsa kusasiyana, kusasalidwa, ndi kuwapatsa mphamvu anthu olumala m’Malawi muno. Bukhu lino lotchedwa Mtanthauzira mawu wa Chiyankhulo cha Manja cha chiMalawi likusindikizidwa pa nthawi yoyenera pozindikira kuti, posachedwapa, Boma lasindikiza Chikonzero Chokwaniritsira Ntchito Yowonetsetsa kuti Zinthu Zonse Zochitika Mdziko Muno Zikuchitika Moganizira Olumala (National Disability Mainstreaming Strategy and Implementation Plan (2018-2023), m’chingelezi). Chikonzerochi chikupereka nsanamira zolimbikitsira ntchito zachitukuko zotsogoleredwa ndi ndondomeko za boma zomwe zimaganizira ufulu ndi zosowa zokhudza chitukuko za anthu olumala. Kotero, ino ndi nthawi yakuti anthu onse okhala ndi ulumali wosamva, pamodzi ndi ena onse, ayenera kugwiritsa chiyankhulo cha manja pofuna kukwaniritsa zosowa za anthu okhala ndi ulumaliwu pofuna kuwonesetsa kuti ntchito zachitukuko zokukomera aliyense.

Chiyankhulo ndi kulumikizana muzochitika ndizofunika kwambiri m’moyo wa tsiku ndi tsiku. Izi ndizofunukira kwambiri potilora kuti ife tithe kukhala moyo wabwino pokhala ndi anzathu ndi m’mene ife timamvera muntima zinthu zikamachitika, komanso pokambirana ndi kuphunzira zina ndi zina. Nkofunika kwambiri kusalora ulumali wakusamva kulepheretsa anthu okhala ndi ulumaliwu kulumikizana ndi ena. Chiyankhulo cha manja ndi chida chapamwamba kwambiri chomwe chikhonza kuthetsa kulephera kulumikizana komwe kumadza chifukwa cha ulumali osamva. Boma lathu limalimbikitsa nzika iri yonse kuti iphunzire chiyankhulo cha manja, pozindikira kuti kulumikizana pakati pa anthu ndi chinthu chokhazikika pamene pali anthu, ndipo izi zimapangitsa kuphunzira chiyankhulo cha manjachi kukhala chinthu chofunikira kwambiri pankhani yakulumikizana.

Kusapezeka ndi kugwiritsidwa ntchito mosayenera kwa chiyankhulo cha manjachi kuli ndi kuthekera kowapanga anthu omwe ali ndi ulumali osamva kukhala otalikirana ndi chitukuko chifukwa chosowa maphunziro, kusakwanira kwa njira zomwe angaphunzirire chiyankhulochi, njira zosakwanira bwino zomasulira chiyankhulochi, ndi kuchepa kwa mwayi wa ntchito pakati pa anthu omwe ali ndi ulumaliwu. Izi ziri chonchi chifukwa chakuti anthu alunga amatenga ulumali osamva ngati chofooka, chinthu chomwe chikusoweka kuchitapo kanthu. Komabe, pakati pa mawonedwe azinthu olakwikawa, Mtanthauzira mawuyu wakonzedwa ndi anthu okhala ndi ulumali osamva mogwirizana ndi akadaulo osiyanasiyana a mdziko muno ndi a kunja. Kotero vuto lokhudza kulumikizana ladza chifukwa cha ulumali wa kusamva likhonza kuchepetsedwa ngati anthu omwe ali ndi ulumaliwu akuthandizidwa ndi ife tonse ndi pamene akupatsidwa zonse zowayenereza.

Boma, mogwirizana ndi mabugwe ake pa ntchito za chitukuko a mdziko muno ndi a kunja, liyesetsa kupereka zonse zofunikira kuti mtanthuzirayu agwiritsidwe ntchito mokwanira ndi mopindulira anthu omwe ali ndi ulumali osamva komanso alunga. Koma, ngakhale mtanthauzira mawuyu ali chinthu cha mtengo wapatali, chobetchera nchakuti anthu omwe ali ndi ulumali wosamva ayambe kudziwona mwatsopano posiya kukhala olandira thandizo loperekedwa kwa anthu osowa ndi kuyamba kukhala anthu amachitachita pa maphunziro, zolemba anthu ntchito, ndi zochitika zokhudza magulu a anthu, mwa zina, kuti tonse, limodzi, tithe kusintha Malawi kuti nzika iriyonse ithe kusangalala ndi moyo.

Boma la Malawi ndi lothokoza kwambiri Boma la Finland kudzera mu Bungwe la Anthu Omwe ali ndi Ulumali Osamva mu Dziko la Finland (Finnish Association of the Deaf, mu Chingerezi) chifukwa cha upangiri ndithandizo la chuma zomwe zatheketsa kusindikizidwa koyamba kwa mtanthauzira mawuyu.


Dr. Lazarus McCarthy Chakwera
Mtsogoleri wa Dziko la Malawi

To top